1 Usabvutike mtima cifukwa ca ocita zoipa,Usacite nsanje cifukwa ca ocita cosalungama.
2 Pakuti adzawamweta msanga monga udzu,Ndipo adzafota monga msipu wauwisi.
3 Khulupirira Yehova, ndipo cita cokoma;Khala m'dziko, ndipo tsata coonadi.
4 Udzikondweretsenso mwa Yehova;Ndipo iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.
5 Pereka njira yako kwa Yehova; Khulupiriranso Iye, adzacicita.
6 Ndipo adzaonetsa cilungamo cako monga kuunika,Ndi kuweruza kwako monga usana.
7 Khala cete mwa Yehova, numlindirire Iye:Usabvutike mtima cifukwa ca iye wolemerera m'njira yace,Cifukwa ca munthu wakucita ciwembu.