15 Lupanga lao lidzalowa m'mtima mwao momwe,Ndipo mauta ao adzatyoledwa.
16 Zocepa zace za wolungama zikomaKoposa kucuruka kwao kwa oipa ambiri.
17 Pakuti manja a oipa adzatyoledwa:Koma Yehova acirikiza olungama.
18 Yehova adziwa masiku a anthu angwiro:Ndipo cosiyira cao cidzakhala cosatha.
19 Sadzacita manyazi m'nyengo yoipa:Ndipo m'masiku a njala adzakhuta.
20 Pakuti oipa adzatayika,Ndipo adani ace a Yehova adzanga mafuta a ana a nkhosa:Adzanyeka, monga utsi adzakanganuka.
21 Woipa akongola, wosabweza:Koma wolungama acitira cifundo, napereka.