22 Pakuti iwo amene awadalitsa adzalandira dziko lapansi;Koma iwo amene awatemberera adzadulidwa.
23 Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu;Ndipo akondwera nayo njira yace.
24 Angakhale akagwa, satayikiratu:Pakuti Yehova agwira dzanja lace.
25 Ndinali mwana ndipo ndakalamba:Ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa,Kapena mbumba zace zirinkupempha cakudya.
26 Tsiku lonse acitira cifundo, nakongoletsa;Ndipo mbumba zace zidalitsidwa.
27 Siyana naco coipa, nucite cokoma,Nukhale nthawi zonse.
28 Pakuti Yehova akonda ciweruzo,Ndipo sataya okondedwa ace:Asungika kosatha:Koma adzadula mbumba za oipa.