24 Angakhale akagwa, satayikiratu:Pakuti Yehova agwira dzanja lace.
25 Ndinali mwana ndipo ndakalamba:Ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa,Kapena mbumba zace zirinkupempha cakudya.
26 Tsiku lonse acitira cifundo, nakongoletsa;Ndipo mbumba zace zidalitsidwa.
27 Siyana naco coipa, nucite cokoma,Nukhale nthawi zonse.
28 Pakuti Yehova akonda ciweruzo,Ndipo sataya okondedwa ace:Asungika kosatha:Koma adzadula mbumba za oipa.
29 Olungama adzalandira dziko lapansi,Nadzakhala momwemo kosatha.
30 Pakamwa pa wolungama palankhula zanzeru,Ndi lilime lace linena ciweruzo.