37 Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima!Pakuti ku matsiriziro ace a munthuyo kuti mtendere.
38 Koma olakwa adzaonongeka pamodzi:Matsiriziro a oipa adzadutidwa.
39 Koma cipulumutso ca olungama cidzera kwa Yehova,Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso.
40 Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa:Awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa,Cifukwa kuti anamkhulupirira Iye,