8 Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo:Usabvutike mtima ungacite coipa,
9 Pakuti ocita zoipa adzadulidwa:Koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.
10 Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti:Inde, udzayang'anira mbuto yace, nudzapeza palibe.
11 Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi;Nadzakondwera nao mtendere wocuruka.
12 Woipa apangira ciwembu wolungama,Namkukutira mano.
13 Ambuye adzamseka:Popeza apenya kuti tsiku lace likudza.
14 Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao;Alikhe ozunzika ndi aumphawi,Aphe amene ali oongoka m'njira: