15 Pakuti ndikuyembekezani Inu, Yehova;Inu mudzayankha, Ambuye Mulungu wanga.
16 Pakuti ndinati, Asakondwerere ine:Pakuterereka phazi langa, asadzikuze pa ine.
17 Ndafikana potsimphina;Ndipo cisoni canga ciri pamaso panga cikhalire.
18 Pakuti ndidzafotokozera mphulupulu yanga;Nditenga nkhawa cifukwa ca chimo langa.
19 Koma adani anga ali ndi moyo, nakhalandi mphamvu:Ndipo akundida kopanda cifukwa acuruka.
20 Ndipo iwo akubwezera coipa pa cabwinoAtsutsana nane, popeza nditsata cabwino.
21 Musanditaye, Yehova:Mulungu wanga, musakhale kutali ndi ine.