1 Pakupfuula ine mundiyankhe, Mulungu wa cilungamo canga;Pondicepera mwandikulitsira malo:Ndicitireni cifundo, imvani pemphero langa.
2 Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti?Mudzakonda zacabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti?
3 Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayoAdzamva Yehova m'mene ndimpfuulira Iye,
4 Citani cinthenthe, ndipo musacimwe:Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale cete.
5 Iphani nsembe za cilungamo,Ndipo mumkhulupirire Yehova.