5 Iphani nsembe za cilungamo,Ndipo mumkhulupirire Yehova.
6 Ambiri amati, Adzationetsa cabwino ndani?Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.
7 Mwapatsa cimwemwe mumtima mwanga,Cakuposa cao m'nyengo yakucuruka dzinthu zao ndi vinyo wao.
8 Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo;Cifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.