1 Kuyembekeza ndayembekeza Yehova;Ndipo anandilola, namva kupfuula kwanga.
2 Ndipo anandikweza kunditurutsa m'dzenje la citayiko, ndi m'thope la pacithaphwi;Nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.
3 Ndipo anapatsa Nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, cilemekezo ca kwa Mulungu wanga;Ambiri adzaciona, nadzaopa,Ndipo adzakhulupirira Yehova.
4 Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika;Wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza.