1 Wodala iye amene asamalira wosauka:Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa:
2 Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, ndipo adzadalitsika pa dziko lapansi;Ndipo musampereke ku cifuniro ca adani ace.
3 Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira;Podwala iye mukonza pogona pace,
4 Ndinati ine, Mundicitire cifundo, Yehova:Ciritsani mtima wanga; pakuti ndacimwira Inu.