2 Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, ndipo adzadalitsika pa dziko lapansi;Ndipo musampereke ku cifuniro ca adani ace.
3 Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira;Podwala iye mukonza pogona pace,
4 Ndinati ine, Mundicitire cifundo, Yehova:Ciritsani mtima wanga; pakuti ndacimwira Inu.
5 Adani anga andinenera coipa, ndi kuti,Adzafa liti, ndi kutayika dzina lace?
6 Ndipo akadza kundiona wina angonena bodza;Mumtima mwace adzisonkhera zopanda pace:Akamka nayenda namakanena:
7 Onse akudana nane andinong'onezerana;Apangana condiipsa ine.
8 Camgwera cinthu coopsa, ati;Popeza ali gonire sadzaukanso.