9 Ngakhale bwenzi langa leni leni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga,Anandikwezera cidendene cace.
10 Koma Inu, Yehova, mundicitire cifundo, ndipo mundiutse,Kuti ndiwabwezere.
11 Umo ndidziwa kuti mukondwera ndi ine,Popeza mdani wanga sandiseka.
12 Ndipo ine, mundigwirizize m'ungwiro wanga,Ndipo mundiike pankhope panu ku nthawi yamuyaya.
13 Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israyeli,Kucokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha.Amen, ndi Amen.