14 Mutiika tikhale onyozeka mwa amitundu,Ndi kuti anthu atipukusire mitu.
15 Tsiku lonse cimpepulo canga cikhala pamaso panga,Ndipo manyazi a pankhope panga andikuta.
16 Cifukwa ca mau a wotonza wocitira mwano;Cifukwa ca mdani ndi wobwezera cilango,
17 Zonsezi zatigwera; koma sitinakuiwalani,Ndipo sitinacita monyenga m'pangano lanu.
18 Mtima wathu sunabwerera m'mbuyo,Ndipo m'mayendedwe athu sitinapatuka m'njira yanu;
19 Mungakhale munatityola mokhala zirombo,Ndi kutiphimba nao mthunzi wa imfa.
20 Tikadaiwala dzina la Mulungu wathu,Ndi kutambasulira manja athu kwa mulungu wacilendo;