3 Pakuti sanalanda dziko ndi lupanga lao,Ndipo mkono wao sunawapulumutsa:Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu.Popeza munakondwera nao,
4 Inu ndinu mfumu yanga, Mulungu:Lamulirani cipulumutso ca Yakobo.
5 Mwa Inu tidzakankhira pansi otsutsana nafe:M'dzina lanu tidzapondereza akutiukira ife.
6 Pakuti sinditama uta wanga,Ndipo lupanga langa silingandipulumutse.
7 Koma Inu munatipulumutsa kwa iwo akutsutsana nafe,Ndipo akudana nafe, mudawacititsa manyazi.
8 Mwa Mulungu tidzitamanda tsiku lonse,Ndipo dzina lanu tidzaliyamika kosatha.
9 Koma mwatitaya, ndi kutinyazitsa;Ndipo simuturuka nao makamu a nkhondo athu.