9 Koma mwatitaya, ndi kutinyazitsa;Ndipo simuturuka nao makamu a nkhondo athu.
10 Mutibwereretsa kuthawa otisautsa:Ndipo akudana nafe adzifunkhira okha.
11 Mwatipereka ngati nkhosa zoyenera kuzidya;Ndipo mwatibalalitsa mwa amitundu.
12 Mugulitsa anthu anu kwacabe,Ndipo mtengo wace simupindula nao.
13 Mutisandutsa cotonza kwa anzathu,Ndi coseketsa ndi colalatitsa iwo akutizinga.
14 Mutiika tikhale onyozeka mwa amitundu,Ndi kuti anthu atipukusire mitu.
15 Tsiku lonse cimpepulo canga cikhala pamaso panga,Ndipo manyazi a pankhope panga andikuta.