1 Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu,Thandizo lopezekeratu m'masautso.
2 Cifukwa cace sitidzacita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi,Angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja;
3 Cinkana madzi ace akokoma, nacita thobvu,Nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwace.
4 Pali mtsinje, ngalande zace zidzakondweretsa mudzi wa Mulungu.Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba,
5 Mulungu ali m'kati mwace, sudzasunthika:Mulungu adzauthandiza mbanda kuca.