2 Cifukwa cace sitidzacita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi,Angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja;
3 Cinkana madzi ace akokoma, nacita thobvu,Nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwace.
4 Pali mtsinje, ngalande zace zidzakondweretsa mudzi wa Mulungu.Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba,
5 Mulungu ali m'kati mwace, sudzasunthika:Mulungu adzauthandiza mbanda kuca.
6 Amitundu anapokosera; maufumu anagwedezeka:Ananena mau, dziko lapansi linasungunuka.
7 Yehova wa makamu ali ndi ife;Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.
8 Idzani, penyani nchito za Yehova,Amene acita zopululutsa pa dziko lapansi.