7 Yehova wa makamu ali ndi ife;Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.
8 Idzani, penyani nchito za Yehova,Amene acita zopululutsa pa dziko lapansi.
9 Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi;Athyola uta, nadula nthungo;Atentha magareta ndi moto.
10 Khalani cete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu:Ndidzabuka mwa amitundu,Ndidzabuka pa dziko lapansi.
11 Yehova wa makamu ali ndi ife,Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu,