1 Ombani m'manja, mitundu yonse ya anthu;Pfuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuyimbitsa.
2 Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa;Ndiye mfumu yaikuru pa dziko lonse lapansi.
3 Atigonjetsera anthu,Naika amitundu pansi pa mapazi athu.
4 Atisankhira colowa cathu,Cokometsetsa ca Yakobo amene anamkonda.
5 Mulungu wakwera ndi mpfuu,Yehova ndi liu la lipenga.