2 Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa;Ndiye mfumu yaikuru pa dziko lonse lapansi.
3 Atigonjetsera anthu,Naika amitundu pansi pa mapazi athu.
4 Atisankhira colowa cathu,Cokometsetsa ca Yakobo amene anamkonda.
5 Mulungu wakwera ndi mpfuu,Yehova ndi liu la lipenga.
6 Yimbirani Mulungu, yimbirani;Yimbirani Mfumu yathu, yimbirani.
7 Pakuti Mulungu ndiye Mfumu ya dziko lonse lapansi;Yimbirani ndi cilangizo.
8 Mulungu ndiye Mfumu ya amitundu:Mulungu akhala pa mpando wacifumu wace woyera.