1 Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi,M'mudzi wa Mulungu wathu, m'phiri lace loyera.
2 Phiri la Ziyoni, cikhalidwe cace ncokomaKu mbali zace za kumpoto,Ndilo cimwemwe ca dziko lonse lapansi,Mudzi wa mfumu yaikuru.
3 Mulungu adziwika m'zinyumba zace ngati msanje.
4 Pakuti, taonani, mafumuwo anasonkhana,Anapitira pamodzi.
5 Anapenya mudziwo, ndipo pamenepo anadabwa;Anaopsedwa, nathawako.
6 Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira;Anamva cowawa, ngati wam'cikuta.
7 Muswa zombo za ku Tarisi ndi mphepo ya kum'mawa.