10 Monga dzina lanu, Mulungu,Momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi:M'dzanja lamanja lanu mudzala cilungamo.
11 Likondwere phiri la Ziyoni,Asekere ana akazi a Yuda,Cifukwa ca maweruzo anu.
12 Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge;Werengani nsanja zace.
13 Penyetsetsani malinga ace,Yesetsani zinyumba zace;Kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m'mbuyo.
14 Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu ku nthawi za nthawi:Adzatitsogolera kufikira imfa.