7 Muswa zombo za ku Tarisi ndi mphepo ya kum'mawa.
8 Monga tidamva, momwemo tidapenyaM'mudzi wa Yehova wa makamu, m'mudzi wa Mulungu wathu:Mulungu adzaukhazikitsa ku nthawi yamuyaya.
9 Tidalingalira za cifundo canu, Mulungu,M'kati mwa Kacisi wanu.
10 Monga dzina lanu, Mulungu,Momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi:M'dzanja lamanja lanu mudzala cilungamo.
11 Likondwere phiri la Ziyoni,Asekere ana akazi a Yuda,Cifukwa ca maweruzo anu.
12 Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge;Werengani nsanja zace.
13 Penyetsetsani malinga ace,Yesetsani zinyumba zace;Kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m'mbuyo.