1 Udzitamandiranji ndi coipa, ciphonaiwe?Cifundo ca Mulungu cikhala tsiku lonse.
2 Lilime lako likupanga zoipa;Likunga lumo lakuthwa, lakucita monyenga.
3 Ukonda coipa koposa cokoma;Ndi bodza koposa kunena cilungamo.
4 Ukonda mau onse akuononga, Lilime lacinyengo, iwe.