1 Ndipulumutseni, Mulungu, mwa dzina lanu,Ndipo mundiweruze ndi mphamvuyanu.
2 Imvani pemphero langa, Mulungu;Cherani khutu mau a pakamwa panga.
3 Pakuti alendo andiukira,Ndipo oopsa afunafuna moyo wanga;Sadziikira Mulungu pamaso pao.
4 Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga:Ambuye ndiye wacirikiza moyo wanga.
5 Adzabwezera coipa adani anga:Aduleni m'coonadi canu.