2 Imvani pemphero langa, Mulungu;Cherani khutu mau a pakamwa panga.
3 Pakuti alendo andiukira,Ndipo oopsa afunafuna moyo wanga;Sadziikira Mulungu pamaso pao.
4 Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga:Ambuye ndiye wacirikiza moyo wanga.
5 Adzabwezera coipa adani anga:Aduleni m'coonadi canu.
6 Ine mwini ndidzapereka nsembe kwa Inu:Ndidzayamika dzina lanu, Yehova, pakuti nlokoma.
7 Pakuti anandilanditsa m'nsautso yonse;Ndipo ndapenya ndi diso langa ico ndakhumbira pa adani anga,