14 Tinapangirana upo wokoma,Tinaperekeza khamu la anthu popita ku nyumba ya Mulungu.
15 Imfa iwagwere modzidzimutsa,Atsikire kumanda ali amoyo:Pakuti m'mokhala mwao muli zoipa pakati pao,
16 Koma ine ndidzapfuulira kwa Mulungu;Ndipo Yehova atizandipulumutsa.
17 Madzulo, m'mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula,Ndipo adzamva mau anga.
18 Anaombola moyo wanga ku nkhondo yondilaka, ndikhale mumtendere:Pakuti ndiwo ambiri okangana nane.
19 Mulungu adzamva, nadzawasautsa,Ndiye wokhalabe ciyambire kale lomwe.Popeza iwowa sasinthika konse,Ndipo saopa Mulungu.
20 Anaturutsa manja ace awagwire iwo akuyanjana naye:Anaipsa pangano lace.