5 Mantha ndi kunjenjemera zandidzera,Ndipo zoopsetsa zandikuta.
6 Ndipo ndinati, Ha, wina akadandipatsa mapiko onga a njiwaMwenzi nditauluka, ndi kukhaliratu.
7 Onani, ndikadathawira kutari,Ndikadagona m'cipululu.
8 Ndikadafulumira ndipulumukeKu mphepo yolimba ndi namondwe.
9 Aonongeni, Ambuye, gawani lilime lao:Pakuti ndaona ciwawa ndi ndeu m'mudzimo.
10 Izizo ziuzungulira pa malinga ace usana ndi usiku;Ndipo m'kati mwace muli zapanda pace ndi cobvuta.
11 M'kati mwace muli kusakaza:Ciwawa ndi cinyengo sizicoka m'makwalala ace.