7 Onani, ndikadathawira kutari,Ndikadagona m'cipululu.
8 Ndikadafulumira ndipulumukeKu mphepo yolimba ndi namondwe.
9 Aonongeni, Ambuye, gawani lilime lao:Pakuti ndaona ciwawa ndi ndeu m'mudzimo.
10 Izizo ziuzungulira pa malinga ace usana ndi usiku;Ndipo m'kati mwace muli zapanda pace ndi cobvuta.
11 M'kati mwace muli kusakaza:Ciwawa ndi cinyengo sizicoka m'makwalala ace.
12 Pakuti si mdani amene ananditonzayo;Pakadatero ndikadacilola:Amene anadzikuza pa ine sindiye munthu wondida;Pakadatero ndikadambisalira:
13 Koma ameneyo ndiwe, munthu woyenerana nane,Tsamwali wanga, wodziwana nane.