4 Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ace:Ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa;Anthu adzandicitanji?
5 Tsiku lonse atenderuza mau anga:Zolingirira zao zonse ziri pa ine kundicitira coipa.
6 Amemezana, alalira,Achereza mapazi anga,Popeza alindira moyo wanga.
7 Kodi adzapulumuka ndi zopanda pace?Gwetsani anthu mumkwiyo, Mulungu.
8 Muwerenga kuthawathawa kwanga:Sungani misozi yanga m'nsupa yanu;Kodi siikhala m'buku mwanu?
9 Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine:Ici ndidziwa, kuti Mulungu abvomerezana nane.
10 Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ace:Mwa Yehova ndidzalemekeza mau ace.