9 Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine:Ici ndidziwa, kuti Mulungu abvomerezana nane.
10 Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ace:Mwa Yehova ndidzalemekeza mau ace.
11 Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzaopa;Munthu adzandicitanji?
12 Zowindira Inu Mulungu, ziri pa ine:Ndidzakucitirani zoyamika.
13 Pakuti mwalanditsa moyo wanga kuimfa:Simunatero nao mapazi anga kuti ndingagwe?Kuti ndiyende pamaso pa MulunguM'kuunika kwa amoyo.