1 Kodi muli cete ndithu poyenera inu kunena zolungama?Muweruza ana a anthu molunjika kodi?
2 Inde, mumtima mucita zosalungama;Pa dziko lapansi mugawira anthu ciwawa ca m'manja mwanu.
3 Oipa acita cilendo cibadwire:Asokera kuyambira kubadwa kwao, nanena bodza.
4 Ululu wao ukunga wa njoka;Akunga mphiri yogontha m'khutu, itseka m'khutu mwace.
5 Imene simvera liu la oitana,Akucita matsenga mocenieratu,
6 Tyolani mano ao m'kamwa mwao, Mulungu:Zulani zitsakano za misona ya mkango, Yehova.
7 Apitetu ngati madzi oyenda;Popiringidza mibvi yace ikhale yodukaduka.