8 Apite ngati nkhono yosungunuka;Asaone dzuwa monga mtayo,
9 Miphika yanu isanagwire moto waminga,Adzaiuluza, yaiwisi ndi yoyaka.
10 Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera cilango:Adzasamba mapazi ace m'mwazi wa woipa.
11 Ndipo anthu adzati, Indedi, pali mphotho kwa wolungama;Indedi, pali Mulungu wakuweruza pa dziko lapansi.