1 Ndilanditseni kwa adani anga, Mulungu wanga:Ndiikeni pamsanje kwa iwo akundiukira.
2 Mundilanditse kwa ocita zopanda pace,Ndipo ndipulumutseni kwa anthu olira mwazi.
3 Pakuti onani, alalira moyo wanga;Amphamvu andipangira ciwembu:Osacimwa, osalakwa ine, Yehova,
4 Osawapatsa cifukwa ine, athamanga nadzikonza;Galamukani kukomana nane, ndipo penyani.
5 Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli,Ukani kukazonda amitundu onse:Musacitire cifundo mmodzi yense wakucita zopanda pace monyenga.
6 Abwera madzulo, auwa ngati garu,Nazungulira mudzi.