1 Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,Ndipo musandilange m'ukali wanu.
2 Mundicitire cifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine:Mundicize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.
3 Moyo wanganso wanthunthumira kwakukuru;Ndipo Inu, Yehova, kufikira liti?
4 Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga;Ndipulumutseni cifukwa ca kukoma mtima kwanu.