1 Mwatitaya Mulungu, mwatipasula;Mwakwiya; tibwezereni.
2 Mwagwedeza dziko, mwaling'amba:Konzani ming'alu yace; pakuti ligwedezeka.
3 Mwaonetsa anthu anu zowawa:Mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa.
4 Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu,Aikweze cifukwa ca coonadi.