4 Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu,Aikweze cifukwa ca coonadi.
5 Kuti okondedwa anu alanditsidwe,Pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutibvomereze.
6 Mulungu walankhula m'ciyero cace; ndidzakondwerera:Ndidzagawa Sekemu, ndidzayesa muyeso cigwa ca Sukoti.
7 Gileadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga;Ndipo Efraimu ndi mphamvu ya mutu wanga;Yuda ndiye wolamulira wanga,
8 Moabu ndiye mkhate wanga;Pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga:Filistiya, pfuulatu cifukwa ca ine.
9 Adzandifikitsa ndani m'mudzi wa m'linga?Adzanditsogolera ndani ku Edomu?
10 Si ndinu, Mulungu, amene mwantaya?Osaturuka nao makamu athu, Mulungu.