8 Moabu ndiye mkhate wanga;Pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga:Filistiya, pfuulatu cifukwa ca ine.
9 Adzandifikitsa ndani m'mudzi wa m'linga?Adzanditsogolera ndani ku Edomu?
10 Si ndinu, Mulungu, amene mwantaya?Osaturuka nao makamu athu, Mulungu.
11 Tithandizeni kunsautso;Kuti cipulumutso ca munthu ndi cabe.
12 Mwa Mulungu tidzacita molimbika mtima,Ndipo Iye adzapondereza otisautsa.