1 Moyo wanga ukhalira cete Mulungu yekha:Cipulumutso canga cifuma kwa Iye.
2 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi cipulumutso canga;Msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukuru.
3 Mudzambvumbvulukira munthu mpaka liti,Kumupha iye, nonsenu,Monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka?
4 Komatu amkhaliraupo kuti amkankhire pansi ulemu wace;Akondwera nao mabodza;Adalitsa ndi m'kamwa mwao, Koma atemberera mumtima.