5 Moyo wanga, ukhalire cete Mulungu yekha;Pakuti ciyembekezo canga cifuma kwa Iye,
6 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi cipulumutso canga,Msanje wanga, sindidzagwedezeka.
7 Pa Mulungu pali cipulumutso canga ndi ulemerero wanga:Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu.
8 Khulupirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu:Tsanulirani mitima yanu pamaso pace:Mulungu ndiye pothawirapo ife.
9 Indetu, anthu acabe ndi mpweya, ndipo anthu akuru ndi bodza:Pakuwayesa apepuka;Onse pamodzi apepuka koposa mpweya,
10 Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama cifwamba;Cikacuruka cuma musakhazikepo mitima yanu.
11 Mulungu ananena kamodzi, ndinacimva kawiri:Kuti mphamvu ndi yace ya Mulungu: