9 Indetu, anthu acabe ndi mpweya, ndipo anthu akuru ndi bodza:Pakuwayesa apepuka;Onse pamodzi apepuka koposa mpweya,
10 Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama cifwamba;Cikacuruka cuma musakhazikepo mitima yanu.
11 Mulungu ananena kamodzi, ndinacimva kawiri:Kuti mphamvu ndi yace ya Mulungu:
12 Cifundonso ndi canu, Ambuye:Cifukwa Inu musudzula munthu ali yense monga mwa nchito yace.