1 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kuca:Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu,M'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi.
2 Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu,Monga ndinakuonani m'malo oyera.
3 Pakuti cifundo canu ciposa moyo makomedwe ace;Milomo yanga idzakulemekezani.
4 Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga;Ndidzakweza manja anga m'dzina lanu.