4 Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga;Ndidzakweza manja anga m'dzina lanu.
5 Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona;Ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakupfuula mokondwera;
6 Pokumbukira Inu pa kama wanga,Ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.
7 Pakuti munakhala mthandizi wanga;Ndipo ndidzapfuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.
8 Moyo wanga uumirira Inu:Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.
9 Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge,Adzalowa m'munsi mwace mwa dziko.
10 Adzawapereka ku mphamvu ya lupanga;Iwo adzakhala gawo la ankhandwe.