2 Ndibiseni pa upo wacinsinsi wa ocita zoipa;Pa phokoso la ocita zopanda pace:
3 Amene anola lilime lao ngati lupanga,Napiringidza mibvi yao, ndiyo mau akuwawitsa;
4 Kuponyera wangwiro mobisika:Amponyera modzidzimutsa, osaopa.
5 Alimbikitsana m'cinthu coipa;Apangana za kuchera misampha mobisika;Akuti, Adzaiona ndani?
6 Afunafuna zosalungama; kusanthula, asanthuladi kutha;Cingakhale ca m'kati mwace mwa munthu, ndi mtima wozama.
7 Koma Mulungu adzawaponyera mubvi;Adzalaswa modzidzimutsa,
8 Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa;Onse akuwaona adzawathawa.