7 Koma Mulungu adzawaponyera mubvi;Adzalaswa modzidzimutsa,
8 Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa;Onse akuwaona adzawathawa.
9 Ndipo anthu onse adzacita mantha;Nadzabukitsa cocita Mulungu,Nadzasamalira nchito yace.
10 Wolungama adzakondwera mwa Yehova, nadzakhulupirira Iye;Ndipo oongoka mtima onse adzalemekeza.