1 M'Ziyoni akulemekezani Inu mwacete, Mulungu:Adzakucitirani Inu cowindaci.
2 Wakumva pemphero Inu,Zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.
3 Mphulupulu zinandilaka;Koma mudzafafaniza zolakwa zathu.
4 Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa,Akhale m'mabwalo anu:Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu,Za m'malo oyera a Kacisi wanu.