4 Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa,Akhale m'mabwalo anu:Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu,Za m'malo oyera a Kacisi wanu.
5 Mudzatiyankha nazo zoopsa m'cilungamo,Mulungu wa cipulumutso cathu;Ndinu cikhulupiriko ca malekezero Onse a dziko lapansi,Ndi ca iwo okhala kutali kunyanja:
6 Ndinu amene mukhazikitsa mapiri ndi mphamvu yanu;Pozingidwa naco cilimbiko.
7 Amene atontholetsa kukuntha kwa nyanja, kukuntha kwa mafunde ace,Ndi phokoso la mitundu ya anthu.
8 Ndipo iwo akukhala kumalekezero adzacita mantha cifukwa ca zizindikilo zanu; Mukondweretsa apo paturukira dzuwa, ndi apo lilowera.
9 Muceza nalo dziko lapansi, muhthirira,Mulilemeza kwambiri;Mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi:Muwameretsera tirigu m'mene munakonzera nthaka.
10 Mukhutitsa nthaka yace yolima;Mufafaniza nthumbira zace?Muiolowetsa ndi mbvumbi;Mudalitsa mmera wace.