9 Muceza nalo dziko lapansi, muhthirira,Mulilemeza kwambiri;Mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi:Muwameretsera tirigu m'mene munakonzera nthaka.
10 Mukhutitsa nthaka yace yolima;Mufafaniza nthumbira zace?Muiolowetsa ndi mbvumbi;Mudalitsa mmera wace.
11 Mubveka cakaci ndi ukoma wanu;Ndipo mabande anu akukha zakuca.
12 Akukha pa mabusa a m'cipululu;Ndipo mapiri azingika naco cimwemwe.
13 Podyetsa mpodzaza ndi zoweta;Ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu;Zipfuula mokondwera, inde ziyimbira.