12 Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu;Tinapyola moto ndi madzi; Koma munatifikitsa potitsitsimutsa.
13 Ndidzalowa m'nyumba yanu ndi nsembe zopsereza,Ndidzakucitirani zowinda zanga,
14 Zimene inazichula milomo yanga,Ndinazinena pakamwa panga pasautsika ine.
15 Ndidzakufukizirani nsembe zapsereza zonona,Pamodzi ndi cofukiza ca mphongo za nkhosa;Ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi.
16 Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu,Ndipo ndidzafotokozera zonse anazicitira moyo wanga,
17 Ndinampfuulira Iye pakamwa panga,Ndipo ndinamkuza ndi lilime langa,
18 Ndikadasekera zopanda pace m'mtima mwanga,Ambuye sakadamvera: